A Chilima Atukwana Zamkabudula Pa Meeting:Auza Mkumano ‘Mache*** Anu’

Chilima Atukwana Zamkabudula

Akuluakulu a UTM ati ACHILIMA safanafikebe pokhwima maganizo atatukwana zansalu pagulu pomwe akuluakuluwo anali pa msonkhanano wokambirana ku Mponela.

Meeting imeneyi inachitika tsiku la Sabata pa 20 October ndipo zokambirana zinayamba ndendende nthawi ya 10 koloko mmawa.

Msonkhanano wa m’bindikirowu kunali anamandwa a UTM okwana 28 ndipo amatsogolera zokambirana anali a Patricia Kaliati ndi a Felix Njawala.

Zinthu zinafika pothina a Kaliati atanena kuti registration ya UTM siitheka ndipo mpofunika nkhani ichoke kukhoti. Mmalo mwake pafunika apeze K12 million kuti akahonge anyamata ena kuti awathandize registration mwachinyengo.

A Kaliati anayimbira a Chilima nkuyika foni pa loud speaker kuti anthu onse azimva. A Kaliati anapempha ndalama zomwe gulu linamvana.

Pamenepa a Chilima anayankha mopuma moto wamkwiyo mofuula:

“Kodi chilichonse chofuna ndalama mungoti Saulosi…Saulosi… bwanji kodi? Chibwanacho ndiye chimenechi. Kumangoti Saulosi…Saulosi…Saulosi… Machendeanu nonse! Mwamva?”

Nthawi yomweyo aliyense kuti bzolii, pakamwa yatsaa kusakhulupilira zolaulazo.

Kunali mphindi yachetee kudziko kutadekha ndi chisoni chosaneneka.

Anthuwo atayesera kuzitolera nkuyambanso kuyankhula mpamene a Manganya anatsanzika kuti akuchoka mu UTM.

Iwo anati “Ife tasiya zipani zathu kudzasatsa Chilima malonda ndiye azitukwana chonchi. Ine ndapita.” Ndipo iwo anatuluka nkukwera galimoto yawo nkumapita.

Zisanachitike zachisonizi, a Ralph Kasambara analinso atayimba foni kusanzika kuti asiya ndale za UTM kaamba koti akhala afuna alabadire mulandu wawo komanso kudwala kwawo. Koma mmawu awo omaliza iwo anati akhala akunena kunena kuti registration ya UTM siitheka ngakhale judge atalamula kuti ichitike.

A Chilima apanikizika kwambiri chifukwa zinthu sizikuyenda.

Leave a Reply

Fill in your details below or click an icon to log in:

WordPress.com Logo

You are commenting using your WordPress.com account. Log Out /  Change )

Google photo

You are commenting using your Google account. Log Out /  Change )

Twitter picture

You are commenting using your Twitter account. Log Out /  Change )

Facebook photo

You are commenting using your Facebook account. Log Out /  Change )

Connecting to %s

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.