MCP District Men Gang Up Aganist Chakwera, Calls Him Greedy, Selfish, Liar: Against ‘PP Convention’ Results

Chakwera under Fire

Malawi Congress Party district chairmen have hanged up against Lazarus Chakwera for selling the Party to People’s Party , and sidelining real MCP supporters with people who he gets money from at the expense of the owners of the party.

The district chairmen have expressed their dissatisfaction with the results of the convention which Chakwera called , saying it does not represent the wish of MCP supporters but his selfish motives , and such , they will use the constitution to deal with him .

Chakwera has been branded as a liar, greedy man , an caring , dictators and stubborn, pointing out that if they knew he was like this in 2013, he would not be the MCP president.

Read the statement here
MALAWI CONGRESS PARTY (MCP)
​​​​​​​​`​​​​​​
PRESS STATEMENT BY DISTRICTS CHAIRMEN OF MCP
MAWU OYAMBA
Choyamba ndafuna kuti ndikuyamikeni nonse ochokera kunyumba zosiyasiya zowulutsira mawu amene mwabwera malo ano lero. Lero ndukuyamikani mwapadera chifukwa mukamva kuti atsogoleri a Malawi Congress Party ayitana mumabwera msanga kudzamva zomwe takutengerani. Ndithokozenso atsogoleri amzanga a chipani cha Malawi Congress Party amene muli pompano komanso awo amene sadafike pano chifukwa cha zifukwa zosiyanasiyana koma nsonkhano uno akuwufunira zabwino. Inunso anyamata athu a Youth League komanso Womens League ndukuthokozani kwambiri chifukwa chosatopa mukayitanidwa pa mikumano ngati iyi. M’mbuyomu takhala tikukumana pa madandaulo okhudza Dr. Lazarus Chakwera yemwe tidamusankha ku msonkhano wawukulu wa chipani cha Malawi Congress Party pa 9 August, 2013 kuti atitsogolere. Iwowa akhala akuchita zinthu zambiri zonyazitsa chipanichi monga kuchotsa anthu m’maudindo, kugwira ntchito za chipani ndi anthu amene sali a chipanichi monga Hon. Sidik Mia ndi ena otero. Tonse akuluakulu m’chipanimu takhala tikudabwa kuti kodi a Chakwera akufuna chani kwenikweni. Koma cholinga chawo chenicheni tidachidziwa pamene adanamiza dziko kuti ayitanitsa msonkhano waukulu wa chipano cha Malawi Congress Party pomwe chilungamo chake anali anthu a chipani cha Peoples Party. Ndipo kumeneko tavetsedwa kuti mipando yake adasankhana motere:
• President Dr Lazarus Chakwera
• First Deputy President Sidik Mia (PP)
• Second Deputy President Harry Mkandawire (PP)
• Secretary General Eisenhower Mkaka
• First Deputy Secretary General Gotani Hara (PP)
• Second Deputy Secretary General Salim Bagus (PP)
• Treasure General Dr Albert Mbawala (PP)
• Director of elections Dr. Elias Chakwera
• Organizing Secretary Khumbize Chiponda MP
• Publicity Secretary Rev Maurice Munthali (PP)
• Director of Economics Dr. Cornelius Mwalwanda (PP)
• Director of Stratergic Planning Dr. Ken Zikhale (PP)
• Second Deputy Treasure General Catherine Chisala (PP)
• Second Deputy Political Affairs Patrick Simwaka (PP)
• Second Deputy Recruitment Wazamazama Katatu
• Second Deputy Organizing Secretary Aram Mbeza (PP)
• Second Deputy Economic Affairs Augustine Mtendere (PP)
• Director of International Relations Dr Thomas Bisika (PP)
• Director of Religious Affairs Muhammad Fahad (PP)
• Director of Campaign Maclean Ndafakale (PP)

Izi zikusemphana ndi mayina amene ife anthu a kumudzi timadziwa kuti ndi anthu a Malawi Congress Party party monga:
• Juliana Lunguzi (MP)
• Maxwell Thyolera (MP)
• Lingson Belekanyama (MP)
• Lewis Chakhwantha (MP)
• Joseph Njovuyalema (MP)
• Kusamba Dzonzi (MP)
• Jessie Kabwira (MP)
• Richard Msowoya (MP)
• Jean Sendeza
• Gustave Kaliwo
• Lyton Dzombe
• Eston Kakhome
• Rhino Chphiko (MP)
• Makala Ngozo (MP)
• Moses Khombe
• Robin Lowe (MP)
• Mayi Chirambo

Lero atsogoleri ochokera m’maboma osiyanasiyana kuyambira kum’mwera, pakati mpaka kumpoto takumana pano kuti tiliwuze dziko pa zatsogolo la Malawi Congress Party motsatira zomwe mtsogoleri wa chipanichi adachita kunamiza dziko la Malawi kuti amapanga msonkhano wawukulu wa chipani cha Malawi Congress Party pa 12, 13 mpaka 14 May, 2018. Ife lero ngati eniake chipanichi tasonkhana pano kuti tinene chilungamo kudziko kuti umene uja sunali mkumano wa Malawi Congress Party pa zifukwa izi:
1. National Executive committee yomwe tidasankha ku mkumano wa 9 August, 2013 sidatengepo mbali. Awa ndi maudindo monga Secretary General, First Deputy President, Treasure General and Deputy Treasure General.
2. Madelegetsi aku convention imeneyi kuphatikiza anthu amene amayimira m’maudindo osiyanasiyana ndi anthu a chipani cha Peoples Party kotero kuti sakukhudzidwa ndi china chirichonse cha Malawi Congress Party. M’ndandanda wa maudindo awa ukungosonyezeratu kuti convention imeneyi idali ya Peoples party kuphatiizapo Dr Lazarus Chakwera amene adalowa Peoples Party pa tsikuli.
3. Ndondomeko yoyitanitsira convention ya dzidzidzi ngati m’mene zidakhalira convention imeneyi sidatsatidwe chifukwa ndi theka la makomiti a m’maboma okha amene angayitanitse convention ya dzidzidzi motsata malamulo a chipani pa gawo 40.
4. Ofesi ya Secretary General sidatulutse kalata ina ilionse yoyitana nthumwi kuti zibwere ku convention imeneyi kutanthauza kuti kagulu ka anthu ena amene maganizo awo ndi wofuna kuba chipani kanachita izi mwamseri. Izi zadziwika kwambiri tikamamva kuchokera ku nyumba zowulutsira mawu kuti anthu amkangoyikana m’maudindo mopanda kuvota kuyambira mpando wa President sadapikisane.
5. Akuluakulu achipanichi omwe aliyense amadziwa kuti nga Malawi Congress Party sadapatsidwe nawo mipando ku convention ya mtunduwu.

Chomcho ife atsogoleri a m’maboma tikuyikana convention ya mtundu wotere kuti sikutikhudza ife a Malawi Congress Party. Ife timakhulupirira kuchita zinthu poyera motsatira ngodya zathu zinayi zomwe ndi umodzi, kumvera, kukhulupirika ndi kusunga mwambo.
TSOGOLO LA CHIPANI CHA MALAWI CONGRESS PARTY
Ife tikudziwa bwino lomwe kuti A Dr. Lazarus Chakwera omwe tidawasankha ku convention ya 9 August, 2013 akhala akulingalira zogulitsa chipani cha Malawi Congress Party kwa Hon. Sidik Mia. Ndipo kuti convention yabodza yomwe adapanga kulikulu la Malawi Congress Party kunali kupereka chipanichi Kwa Hon. Sidik Mia. Chomcho tufuna pa msonkhano uno akuluakulu awiriwa adziwe kuti zimenezo sizitheka. Ife takozeka kuchita chotheka kuti tilanditse chipanichi.
Ife atsogoleri a chipani cha Malawi Congress Party takoza ndondomeko ya m’mene tufuna chiyendere chipani kuchokera lerolino:
1. Potsatira gawo 37(5) la malamulo a chipani cha Malawi Congress Party tikugwirizana ndi kulengeza kumene adachita Hon. Gustav Kaliwo Secretary General wa chipani kuti kuyambira pa 12 May, 2018 Rt hon. Richard Msowoya ndi mtsogoleri wongogwirizira wa chipanichi (acting president).
2. A Dr. Lazarus Chakwera asiye kugwiritsa nchito katundu komanso makaka a chipani cha Malawi Congress Party.
3. Hon. Gustav Kaliwo secretary General ayitanitse msonkhano waukulu wa chipanichi komwe mwa zina tikasankhe atsogoleri atsopano.

MAWU OMALIZA
Ife ndife anthu okhumudwa kwambiri kuti munthu amene tidamuyenereza kuti atsogolere chipani ndi munthu wosakhulupirika, wosakonda anthu, wokonda ndalama, wabodza komanso wa chinyengo. Tikanadziwa za munthu wotereyu pa chiyambi sitikadamukhulupirira kumupatsa mpando. Koma ngati apitirize kugwiritsa ntchito katundu wa Malawi Congress Party ife tichita chinachirichonse chotheka kuti tithane naye motsata malamulo a chipani chathu.

Advertisements

Leave a Reply

Fill in your details below or click an icon to log in:

WordPress.com Logo

You are commenting using your WordPress.com account. Log Out /  Change )

Google photo

You are commenting using your Google account. Log Out /  Change )

Twitter picture

You are commenting using your Twitter account. Log Out /  Change )

Facebook photo

You are commenting using your Facebook account. Log Out /  Change )

Connecting to %s

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.